Funso
Kodi Yesu ndi Mulungu? Kodi Yesu ananenapo kuti Iye ndi Mulungu?
Yankho
Yesu sanalembedwepo mu Baibulo kuti anenapo mawu akuti, āIne ndine Mulungu.ā Izi sizikutanthauza, komabe, kuti sanadzitchule kuti Iye ndi Mulungu. Mwachitsanzo mawu a Yesu mu Yohane 10:30, āIne ndi Atate ndife amodzi.ā Tikuyenera kungoona machitidwe a Ayuda pa mawu ake kuti tidziwe kuti amadzitchula Mulungu. Anafuna kumugenda miyala chifukwa cha chifukwa chomwechi. ā⦠inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulunguā (Yohane 10:33). Ayuda anazindikira bwino lomwe zimene Yesu anali kunena ā māmodzi mwa Milungu. Dziwani kuti Yesu samakana kuti amadzitchula Mulungu. Pamene Yesu ananena, āIne ndi Atate ndife amodziā (Yohane 10:30), amanena kuti Iye ndi Atate ndi achikhalidwe chimodzi. Yohane 8:58 ndi chitsanzo china. Yesu anati, āIndetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu, ine ndilipo!ā Kuyankha kwa Ayuda amene anamva mawu awa kunali kutenga miyala ndikumupha Iye chifukwa cha mwano, monga māmene lamulo la Mose liwalamulira iwo kuchita (Levitiko 24:15).
Yohane anabwereza maganizo a Yesu a Māmodzi mwa Milungu: āMawu anali Mulunguā ndi āMawu anasandulika thupiā (Yohane 1:1,14). Ndime zimenezi zikuonetseratu poyera kuti Yesu ndi Mulungu mu Thupi. Machitidwe a Atumwi 20:28 akutiuza kuti, āKhalani otsogolera Mpingo wa Mulungu, umene anagula ndi mwazi wake.ā Ndi ndani amene anagula Mpingo ā Mpingo wa Mulungu ā ndi mwazi wake? Yesu Khristu. Machitidwe a Atumwi 20:28 akunena kuti Yesu anagula Mpingo wake ndi magazi ake. Kotero, Yesu ndi Mulungu!
Thomasi wophunzira wa Yesu ananena kwa Yesu nati, āAmbuye wanga ndi Mulungu wangaā (Yohane 20:28). Yesu sanamukonza iye. Tito 2:13 akutilimbikitsa kudikilira kubwera kwake kwa Mulungu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu (onaninso 2 Petulo1:1). Pa Aheberi 1:8, Atate akunena za Yesu, āKoma ponena za Mwana anati, āMpando wa chifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi, ndipo oyera mtima adzakhala ndodo ya chifumu ya ufumu wanu.ā Atate amafanizira kwa Yesu ngati āMulunguā kuonetsa kuti Yesu ndiyedi Mulungu.
Ku Chivumbulutso, māngelo anauza Mtumwi Yohane kupembedza Mulungu yekha (Chivumbulutso 19:10). Nthawi zambiri mu Malembo Oyera Yesu amalandira matamando (Mateyu 2:11, 14:33, 28:9, 17; Luka 24:52; Yohane 9:38). Samadzudzula anthu chifukwa chakumupembedza Iye. Ngati Yesu sanali Mulungu, akatha kuwauza anthu kuti asamupembedze Iye, monga māmene māngelo ku Chivumbulutso anachitira. Pali ndime zina za Malembo Oyera zambiri zimene zimanena za Yesu kukhala Māmodzi mwa Milungu.
Chifukwa chofunikira kwambiri chakuti Yesu ayenera kukhala Mulungu ndi chakuti ngati sali Mulungu, imfa yake siikadakhala yokwanira kuwombolera machimo a dziko lapansi (1 Yohane 2:2). Munthu wolengedwa, amene Yesu adakakhala akanakhala kuti Iye si Mulungu, sakanalipira chilango cha muyaya choyenera tchimo limene walakwira Mulungu wamuyaya. Ndi Mulungu yekha angalipire chilango cha mtundu umenewu. Ndi Mulungu yekha amene angasenze machimo a dziko lapansi (2 Akolose 5:21), kufa, ndi kuuka, kugonjetsa tchimo ndi imfa.
English
Kodi Yesu ndi Mulungu? Kodi Yesu ananenapo kuti Iye ndi Mulungu?